1
Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano,
ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.
2 Yes. 54.5; Zek. 9.9; Mat. 21.5 Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga;
ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao.
3Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe;
amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.
4 Mas. 35.27 Popeza Yehova akondwera nao anthu ake;
adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.
5Okondedwa ake atumphe mokondwera m'ulemu:
Afuule mokondwera pamakama pao.
6 Aheb. 4.12 Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao,
ndi lupanga lakuthwa konsekonse m'dzanja lao;
7kubwezera chilango akunja,
ndi kulanga mitundu ya anthu;
8kumanga mafumu ao ndi maunyolo,
ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo,
9 Deut. 7.1-2 kuwachitira chiweruzo cholembedwacho.
Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu.
Aleluya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.