CHIVUMBULUTSO 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Lipenga lachisanu, tsoka loyamba

1 Luk. 10.18; Chiv. 1.18 Ndipo mngelo wachisanu anaomba lipenga, ndipo ndinaona nyenyezi yochokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye chifunguliro cha chiphompho chakuya.

2Ndipo anatsegula pa chiphompho chakuya; ndipo unakwera utsi wotuluka m'chiphomphomo, ngati utsi wa ng'anjo yaikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, chifukwa cha utsiwo wa kuchiphomphocho.

3Eks. 10.4Ndipo m'utsimo mudatuluka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko zili ndi mphamvu.

4Chiv. 7.3Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena chabiriwiri chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pamphumi pao ndiwo.

5Chiv. 9.10Ndipo anapatsa ilo mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe ao anali ngati mazunzidwe a chinkhanira, pamene chiluma munthu.

6Yes. 2.19; Yer. 8.3; Chiv. 6.16Ndipo m'masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.

7Yow. 2.4Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolide, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.

8Ndipo anali nalo tsitsi longa tsitsi la akazi, ndipo mano ao anali ngati mano a mikango.

9Yow. 2.5-7Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zachitsulo; ndipo mkokomo wa mapiko ao ngati mkokomo wa agaleta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.

10Chiv. 9.5Ndipo lili nayo michira yofanana ndi ya chinkhanira ndi mbola; ndipo m'michira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.

11Aef. 2.2; Chiv. 9.1Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake m'Chihebri Abadoni, ndi m'Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.

Lipenga lachisanu ndi chimodzi, tsoka lachiwiri

12 Chiv. 8.13 Tsoka loyamba lapita; taonani, akudzanso matsoka awiri m'tsogolomo.

13Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi anaomba lipenga, ndipo ndinamva mau ochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolide lili pamaso pa Mulungu,

14Chiv. 16.12nanena kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pa mtsinje waukulu Yufurate.

15Ndipo anamasulidwa angelo anai, okonzeka kufikira ora ndi tsiku ndi mwezi ndi chaka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu a anthu.

16Ndipo chiwerengero cha nkhondo za apakavalo ndicho zikwi makumi awiri zochulukitsa zikwi khumi; ndinamva chiwerengero chao.

17Yes. 5.28-29Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulufure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao mutuluka moto ndi utsi ndi sulufure.

18Ndi miliri iyi linaphedwa limodzi la magawo atatu a anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulufure, zotuluka m'kamwa mwao.

19Yes. 9.15Pakuti mphamvu ya akavalo ili m'kamwa mwao, ndi m'michira yao; pakuti michira yao ifanana ndi njoka, nikhala nayo mitu, ndipo aipsa nayoyo.

20Deut. 31.29Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalapa ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;

21ndipo sanalapa mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help