1Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu m'Israele, panali munthu Mlevi wogonera kuseri kwa mapiri a Efuremu amene anadzitengera mkazi wamng'ono wa ku Betelehemu-Yuda.
2Koma mkazi wake wamng'ono anachita chigololo akali naye, namchokera kunka kunyumba ya atate wake ku Betelehemu-Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.
3Koma anauka mwamuna wake namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wake, ndi abulu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye kunyumba ya atate wake. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo anakondwera kukomana naye.
4Ndipo mpongozi wake, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko.
5Ndipo kunali, tsiku lachinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kuchoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wake, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite.
6Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Uvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako.
7Ndipo munthuyo ananyamuka kuti amuke; koma mpongozi wakeyo anamkakamiza, nagonanso komweko.
8Nalawirira mamawa tsiku lachisanu kuti amuke, koma atate wa mkaziyo anati, Ulimbitse mtima wako, nulindire lipendeke dzuwa; nadya iwo onse awiri.
9Pamenepo munthuyo ananyamuka kuchoka, iye ndi mkazi wake wamng'ono ndi mnyamata wake; koma mpongozi wake, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kunka ulendo wanu kwanu.
10Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nachoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali abulu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wake wamng'ono.
11Pofika iwo pa Yebusi linalimkulowa dzuwa, ndi mnyamata anati kwa mbuye wake, Tiyeni, tipatukire mudzi uwu wa Ayebusi ndi kugona pomwepa.
12Koma mbuye wake ananena naye, Tisapatukire mudzi wachilendo, wosati wa ana a Israele, koma tipitirire kunka ku Gibea.
13Nati kwa mnyamata wake, Tiyeni, tiyandikire kwinako: tigone m'Gibea, kapena m'Rama.
14Napitirira iwo, nayenda, ndi dzuwa linawalowera pafupi pa Gibea, ndiwo wa Benjamini.
15Mat. 25.43; Aheb. 13.2Napatukirako, kuti alowe nagone ku Gibea; nalowa iye, nakhala pansi m'khwalala la mudziwo, pakuti panalibe wina wowalandira m'nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona.
16Ndipo taonani, munthu nkhalamba anachokera ku ntchito yake kumunda madzulo; munthuyu ndiye wa ku mapiri a Efuremu, nagonera ku Gibea; koma anthu pamenepo ndiwo Abenjamini.
17Pamene anakweza maso ake anaona munthu wa pa ulendoyo m'khwalala la mudzi; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? Ufumira kuti?
18Yos. 18.1; 1Sam. 1.3, 7Ndipo ananena nayo, Tili kuchokera ku Betelehemu-Yuda, kunka ku mbali za mapiri a Efuremu, ndiko ndifumira ine; koma ndidamuka ku Betelehemu-Yuda; ndipo tsopano ndili kumuka kunyumba ya Yehova; koma palibe munthu wondipatsa nyumba.
19Ngakhale udzu ndi chakudya cha abulu athu ziliko; ndi mkate ndi vinyo zilikonso kwa ine ndi kwa mdzakazi wako ndi kwa mnyamata wokhala ndi akapolo ako; kosasowa kanthu.
20Gen. 19.2; 43.23Ndipo nkhalambayo inati, Mtendere ukhale ndi iwe, komatu, zosowa zako zonse ndidzakupatsa ndi ine; pokhapo usagone m'khwalala.
21Gen. 18.4; 24.32Pamenepo anamlonga m'nyumba yake, napatsa abulu chakudya; ndipo iwo anasamba mapazi ao, nadya, namwa.
22Gen. 19.4Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mudziwo, ndiwo anthu otama zopanda pake, anazinga nyumba, nagogodagogoda pachitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Tulutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.
23Ndipo munthu mwini nyumba anawatulukira nanena nao, Iai, abale anga, musachite choipa chotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musachite chopusa ichi.
24Taonani, mwana wanga wamkazi ndiye namwali, ndi mkazi wake wamng'ono siwa; ndiwatulutse iwo, muwachepetse iwo, ndi kuwachitira monga muyesa chokoma; koma mwamuna uyu musamchitire chopusa ichi.
25Koma amunawo sanafune kumvera; motero munthuyu anagwira mkazi wake wamng'ono, natuluka naye kwa iwo kunja; namdziwa iwo, nachita naye zoipa usiku wonse mpaka m'mawa; namlola achoke mbandakucha.
26Nadza mkaziyo, kutacha, nagwa pakhomo pa nyumba ya munthu padali mbuye wake, kufikira kutayera.
27Pamene mbuye wake anauka mamawa, natsegula pakhomo pa nyumba, natuluka kunka ulendo wake, taona, mkazi wake wamng'ono, atagwa pakhomo pa nyumba ndi manja ake pachiundo.
28Ndipo ananena naye, Tauka, timuke; koma panalibe womyankha. Pamenepo anamuika pa bulu; nanyamuka mwamunayo, namka kwao.
291Sam. 11.7Ndipo pofika iye kunyumba kwake, anatenga mpeni, nagwira mkazi wake wamng'onoyo namgawa chiwalochiwalo magawo khumi ndi awiri, namtumiza ku malire onse a Israele.
30Miy. 11.14Ndipo kunali kuti onse amene anachiona anati, Sichinachitika, inde sichinaoneka chotere chiyambire tsiku lokwera ana a Israele kutuluka m'dziko la Ejipito mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.