EKSODO 4 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mose alandira mphamvu yakuchita zodabwitsa

1Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekere iwe.

2Ndipo Yehova ananena naye, Icho nchiyani m'dzanja lako? Nati, Ndodo.

3Ndipo ananena Iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa.

4Koma Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako, nuigwire kumchira; ndipo anatambasula dzanja lake, naigwira, nikhalanso ndodo m'dzanja lake;

5Mose akomana ndi Aroni

27 Eks. 4.14 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye pa phiri la Mulungu, nampsompsona.

28Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira.

29Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akulu onse a ana a Israele;

30ndipo Aroni anawafotokozera mau onse amene Yehova adauza Mose, nachita zizindikiro zija pamaso pa anthu.

31Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help