1 MBIRI 16 - Buku Lopatulika Bible 2014

1

kuti tiyamike dzina lanu loyera,

ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.

36Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele,

kuyambira kosayamba kufikira kosatha.

Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova.

Chihema chosonkhanako chikhala ku Gibiyoni

37Ndipo anasiyako ku likasa la chipangano la Yehova Asafu ndi abale ake, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;

38ndi Obededomu, ndi abale ake makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi atatu; ndi Obededomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa akhale odikira;

391Maf. 3.4ndi Zadoki wansembe, ndi abale ake ansembe, ku Kachisi wa Yehova, pa msanje unali ku Gibiyoni;

40Eks. 29.38-41kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe zopsereza, kosalekeza, m'mawa ndi madzulo, monga mwa zonse zilembedwa m'chilamulo cha Yehova adachilamulira Israele;

41ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, otchulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake nchosatha;

42ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kuchipata.

43Ndipo anachoka anthu onse, yense kunyumba yake, nabwera Davide kudalitsa nyumba yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help