AEFESO Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014

Mau Oyamba Kalata ya Paulo mtumwi yolembera kwa Aefeso ikunena za “makonzedwe a Mulungu…ndi makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko”. (1.10) Kalatayi ndi pempho kwa anthu a Mulungu kuti akhale molingana ndi chikonzero chachikuluchi pofuna kuyanjanitsa mtundu wonse wa anthu kudzera mu umodzi umene upezeka mwa Yesu Khristu.Mu gawo loyamba la buku la Aefeso wolembayo akutambasula mutu wa umodzi wa mpingo pamene akukamba za m'mene Mulungu Atate anasankhira anthu ake, ndipo m'mene iwowo amalandira chikhululukiro cha machimo namasulidwa kuchokera kumachimo kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu. Komanso akukamba za lonjezo lalikulu la Mulungu limene litsimikizidwa ndi Mzimu Woyera. Mu gawo lachiwiri iye akuwadandaulira awerengi ake kuti umodzi wao mwa Khristu uwonekere poyera pa mayendedwe ao ndi pa moyo wao wonse.Mkalatamu akugwiritsa ntchito zifanizo zingapo pofuna kuonetsa umodzi wa anthu a Mulungu mwa Khristu: mpingo uli ngati thupi, ndipo Khristu ali ngati mutu wake; kapenanso ngati nyumba, ndipo Khristu ndiye mwala wokhala pangodya; kapenanso ngati mkazi, ndipo Khristu ndiye mwamuna wake wa mpingo. Kenaka kalatayi ikufotokoza zinthu zinanso zofunikira pamene wolembayo akunena za chisomo cha Mulungu mwa Khristu. Chilichonse chikuyesedwa molingana ndi chikondi, kudzipereka, kukhululukira machimo, chisomo komanso chiyero cha Khristu.Za mkatimuMau oyamba 1.1-2Khristu ndi mpingo 1.3—3.21Moyo watsopano mwa Khristu 4.1—6.20Mau omaliza 6.21-24
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help