2 MBIRI 2 - Buku Lopatulika Bible 2014

Solomoni apangana ndi Hiramu za mirimo ya Kachisi

1 1Maf. 5 Ndipo Solomoni anati alimangire dzina la Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.

2Nawerenga Solomoni amuna zikwi khumi mphambu makumi asanu ndi limodzi osenza mirimo, ndi amuna zikwi makumi asanu ndi atatu otema mitengo m'mapiri, ndi zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kuwayang'anira.

3Ndipo Solomoni anatumiza kwa Huramu mfumu ya Tiro, ndi kuti, Monga momwe munachitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundichitire ine momwemo.

4Eks. 25.30; 30.7; Num. 28.3Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha m'Israele.

5Mas. 135.5Ndipo nyumba nditi ndimangeyi ndi yaikulu; pakuti Mulungu wathu ndiye wamkulu woposa milungu yonse.

61Maf. 8.27; Yes. 66.1Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko?

7Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine m'Yuda ndi m'Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.

8Munditumizirenso mitengo yamikungudza, ndi yamlombwa, ndi yambawa, ya ku Lebanoni; pakuti ndidziwa kuti anyamata anu adziwa kutema mitengo m'Lebanoni; ndipo taonani, anyamata anga adzakhala ndi anyamata anu,

9ndiko kundikonzera mitengo yambirimbiri; pakuti nyumbayi nditi ndiimange idzakhala yaikulu ndi yodabwitsa.

10Ndipo taonani, ndidzawapatsa anyamata anu otema akulikha mitengo miyeso ya tirigu wopuntha zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya barele zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikulu ya vinyo zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikulu ya mafuta zikwi makumi awiri.

111Maf. 10.9Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anayankha ndi kulembera, natumiza kalatayo kwa Solomoni, ndi kuti, Powakonda anthu ake Yehova anakulongani mfumu yao.

12Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.

13Ndipo tsono ndatumiza munthu waluso wokhala nalo luntha, Huramuabi,

141Maf. 7.13-14ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana akazi a Dani, ndipo atate wake ndiye munthu wa ku Tiro, wodziwa kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira chopanga chilichonse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu.

15Ndipo tsono tirigu ndi barele, mafuta ndi vinyo, mbuye wanga wanenazi, azitumize kwa anyamata ake;

16ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.

17Ndipo Solomoni anawerenga alendo onse okhala m'dziko la Israele, monga mwa mawerengedwe aja atate wake Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.

18Ndipo anaika zikwi makumi asanu ndi awiri za iwowa asenze mirimo, ndi zikwi makumi asanu ndi atatu ateme m'mapiri, ndi akapitao zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi agwiritse anthu ntchito.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help