MASALIMO 63 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mtima woliralira kuyanjana ndi MulunguSalimo la Davide; muja anakhala m'chipululu cha Yuda

1 Mas. 42.2 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga;

ndidzakufunani m'matanda kucha.

Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu,

thupi langa lilirira Inu,

m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.

2Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,

monga ndinakuonani m'malo oyera.

3 Mas. 69.16 Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake;

milomo yanga idzakulemekezani.

4 Mas. 28.2 Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga;

ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.

5 Mas. 36.8 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi chonona;

ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani

ndi milomo yakufuula mokondwera.

6 Mas. 119.55 Pokumbukira Inu pa kama wanga,

ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

7 Mas. 17.8 Pakuti munakhala mthandizi wanga;

ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

8Moyo wanga uumirira Inu.

Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

9Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,

adzalowa m'munsi mwake mwa dziko.

10Adzawapereka kumphamvu ya lupanga;

iwo adzakhala gawo la ankhandwe.

11 Luk. 12.15 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;

yense wakulumbirira iye adzatamandira;

pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help