1 Mas. 17.8; 56.1; 63.7; 91.4 Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo;
pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu,
ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu,
kufikira zosakazazo zidzapita.
2 Mas. 138.8 Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba;
ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.
3 Mas. 56.2 Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa
ponditonza wofuna kundimeza;
Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.
4Moyo wanga uli pakati pa mikango;
ndigona pakati pa oyaka moto,
ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi,
ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthawa.
5 Mas. 108.5 Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu;
ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6 Mas. 7.15 Ananditchera ukonde apo ndiyenda;
moyo wanga wawerama.
Anandikumbira mbuna patsogolo panga;
anagwa m'kati mwake iwo okha.
7 Mas. 108.1-5 Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;
ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.
8Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze!
Ndidzauka ndekha mamawa.
9Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye,
ndidzakuimbirani mwa mitundu.
10 Mas. 103.11 Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba,
ndi choonadi chanu kufikira mitambo.
11 Mas. 57.5 Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu;
ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.