LEVITIKO 14 - Buku Lopatulika Bible 2014

Malamulo a pa kumyeretsa wakhate

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,

2Mat. 8.4; Mrk. 1.44; Luk. 5.14; 17.14Chilamulo cha wakhate tsiku la kumyeretsa kwake ndi ichi: azidza naye kwa wansembe;

3ndipo wansembe atuluke kunka kunja kwa chigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda yakhate yapola pa wakhateyo;

4pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope;

5ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda;

6natenge mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, naziviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;

72Maf. 5.10, 14nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lake, namutche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.

8Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.

9Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lake lonse la pamutu pake, ndi ndevu zake, ndi nsidze zake, inde amete tsitsi lake lonse; natsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nakhale woyera.

10Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.

11Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako;

12ndipo wansembe atenge mwanawankhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yopalamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

13Ndipo akaphere mwanawankhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, pa malo popatulika; pakuti monga nsembe yauchimo momwemo nsembe yopalamula nja wansembe; ndiyo yopatulika kwambiri.

14Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;

15ndipo wansembe atengeko muyeso uja wa mafuta, nawathire pa chikhato cha dzanja lake lamanzere la iye mwini;

16ndipo wansembe aviike chala chake cha dzanja lake lamanja cha iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lake lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi chala chake pamaso pa Yehova;

17ndipo wansembe apakeko mafuta okhala m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yopalamula;

18natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova.

19Ndipo wansembe apereke nsembe yauchimo, namchitire chomtetezera amene akuti ayeretsedwe, chifukwa cha kudetsedwa kwake; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza;

20ndipo wansembe atenthe nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa pa guwa la nsembe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala iye woyera.

21Ndipo akakhala waumphawi chosafikana chuma chake azitenga mwanawankhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yopalamula, aiweyule kumchitira chomtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi magawo atatu wa mafuta;

22ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza.

23Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kuti ayeretsedwe.

24Ndipo wansembe atenge mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndi muyeso uja wa mafuta, ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova;

25naphe mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;

26ndipo wansembe athireko mafuta aja m'chikhato chake chamanzere cha iye mwini;

27ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lake lamanzere ndi chala chake cha dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova;

28ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula;

29ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumchitira chomtetezera pamaso pa Yehova.

30Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo,

31limodzi la nsembe yauchimo, ndi lina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova iye wakuyeretsedwa.

32Ichi ndi chilamulo cha iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pake.

33Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

34Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu;

35pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m'nyumba.

36Ndipo wansembe aziuza kuti atulutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse zili m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;

37naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m'makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ake yakumba kubzola khoma;

38pamenepo wansembe azituluka ku khomo la nyumba, natseka nyumbayo masiku asanu ndi awiri;

39ndipo wansembe abwerenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonenso, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'makoma a nyumba;

40pamenepo wansembe auze kuti agumule miyalayi pali nthenda, naitayire ku malo akuda kunja kwa mudzi;

41napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako;

42natenge miyala ina, naikhazike m'malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo.

43Ndipo ikabweranso nthenda, nibukanso m'nyumba atagumula miyala, ndipo atapala m'nyumba namatanso;

44pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'nyumba, ndiyo khate lonyeka m'nyumba; ndiyo yodetsedwa.

45Ndipo apasule nyumbayo, miyala yake, ndi mitengo yake, ndi dothi lake lonse kumudzi kuzitaya ku malo akuda.

46Ndiponso iye wakulowa m'nyumba masiku ake ili yotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

47Ndipo iye wakugona m'nyumbayo atsuke zovala zake; ndi iye wakudya m'nyumbayo atsuke zovala zake.

48Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aitche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.

49Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo;

50naphe mbalame imodzi m'mbale yadothi, pamwamba pa madzi oyenda;

51natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, naziviike m'mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m'madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m'nyumba;

52nayeretse nyumba ndi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.

53Koma ataye mbalame yamoyo kunja kwa mudzi kuthengo koyera; motero aichitire choitetezera nyumbayo; ndipo idzakhala yoyera.

54Ichi ndi chilamulo cha nthenda iliyonse yakhate, ndi yamfundu;

55ndi ya khate la chovala, ndi la nyumba;

56ndi yachotupa, ndi yankhanambo, ndi yachikanga;

57kulangiza tsiku loti chikhala chodetsa, ndi tsiku loti chikhala choyera; ichi ndi chilamulo cha khate.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help