YESAYA 19 - Buku Lopatulika Bible 2014

Aneneratu za Ejipito

1 Eks. 12.12; Mas. 104.3; Yer. 46.13-26; Ezk. 29—30 Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.

2Ower. 7.22Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mudzi kumenyana ndi mudzi, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.

3Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.

4Ndipo ndidzapereka Ejipito m'manja mwa mbuye wankharwe; ndi mfumu yaukali idzawalamulira, ati Ambuye, Yehova wa makamu.

5Ndipo madzi adzaphwa m'nyanja yaikulu, ndipo nyanja yoyendamo madzi idzaphwa, niuma.

62Maf. 19.24Ndipo nyanja zidzanunkha; mitsinje ya Ejipito idzachepa, nuima; bango ndi mlulu zidzafota.

7Madambo oyandikana ndi Nailo, pafupi ndi gombe la Nailo, ndi zonse zobzala pa Nailo zidzauma, nizichotsedwa, zosakhalanso konse.

8Asodzinso adzalira, ndi onse oponya mbedza m'Nailo adzaliralira, ndi onse oponya makoka m'madzi, adzalefuka.

9Komanso iwo amene agwira ntchito yakupala thonje, ndi iwo amene aomba nsalu yoyera, adzakhala ndi manyazi.

10Ndipo maziko ake adzasweka, onse amene agwira ntchito yolipidwa adzavutidwa mtima.

11Akalonga a Zowani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?

121Ako. 1.20Nanga tsopano anzeru ali kuti? Akuuze iwe tsopano; adziwe chimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kuchitira Ejipito.

13Akalonga a Zowani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asocheretsa Ejipito, amene ali mwala wa pangodya wa mafuko ake.

141Maf. 22.22Yehova wasanganiza mzimu wa kusaweruzika pakati pake; ndipo iwo asocheretsa Ejipito m'ntchito zake zonse, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pake.

15Ejipito sadzakhala ndi ntchito, imene mutu pena mchira, pena nthambi ya kanjedza, pena mlulu zidzaigwira.

16 Yer. 51.30 Tsiku limenelo Ejipito adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, chifukwa cha kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pake.

17Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Ejipito, yense wakulitchula adzamtembenukira mwamantha, chifukwa cha uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga pa dzikolo.

18 Zef. 3.9 Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Ejipito yolankhula chinenero cha Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzatchedwa, Mudzi wa chionongeko.

19Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati pa dziko la Ejipito, ndi choimiritsa cha Yehova m'malire ake.

20Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Ejipito; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, chifukwa cha osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.

21Mala. 1.11Ndipo Yehova adzadziwika kwa Ejipito, ndipo Aejipito adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kuchitadi.

22Ndipo Yehova adzakantha Ejipito kukantha ndi kuchiritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawachiritsa.

23 Yes. 11.16; Zef. 3.9 Tsiku limenelo padzakhala khwalala lochokera m'Ejipito kunka ku Asiriya, ndipo Mwasuri adzafika ku Ejipito, ndi Mwejipito adzafika ku Asiriya, ndipo Aejipito adzapembedzera pamodzi ndi Aasiriya.

24Tsiku limenelo Israele ndi Ejipito ndi Asiriya atatuwa, adzakhala mdalitso pakati pa dziko lapansi;

25Hos. 2.23pakuti Yehova wa makamu wadalitsa iwo, ndi kuti, Odalitsika Ejipito anthu anga, ndi Asiriya ntchito ya manja anga, ndi Israele cholowa changa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help