1 Tit. 3.1; Yoh. 19.11 Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.
2Tit. 3.1; Yoh. 19.11Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.
3Yak. 4.12Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m'menemo:
4pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.
51Pet. 2.19Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbu mtima.
6Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi.
7Mat. 22.21Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.
Kukondana, kudikira, chiyero8 Lev. 19.13; Miy. 3.27-28; Aro. 13.10; Agal. 5.14 Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.
9Eks. 20.13-17; Lev. 19.18; Mat. 22.39-40Pakuti ili, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina lililonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.
10Lev. 19.18; Mat. 22.39-40Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo.
11 Aef. 5.14 Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira.
12Akol. 3.8; Aef. 6.13Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika.
13Miy. 23.20; Yak. 3.14Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.
14Agal. 3.27Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.