1
29Yesu aikidwa m'manda(Mat. 27.57-66; Luk. 23.50-56; Yoh. 19.38-42)
42Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo pa Sabata,
43Luk. 2.25, 38anadzapo Yosefe wa ku Arimatea, mkulu wa milandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wake wa Yesu.
44Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.
45Ndipo pamene anachidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe mtembowo.
46Luk. 23.53Ndipo anagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m'bafutamo, namuika m'manda osemedwa m'thanthwe; nakunkhunizira mwala pakhomo la manda.
47Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.