ZEFANIYA Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014
Mau OyambaIyeyu adalalika mau ake pa nthawi imene mfumu Yosiya anali pafupi kukhazikitsa malamulo oongolera zinthu mu ufumu wake (621 BC.) Bukuli lili ndi mitu yosiyanasiyana ya mauthenga a uneneri monga: tsiku la chiweruzo ndi chiwonogeko, pamene Yuda adzalangidwe chifukwa chopembedza milungu ina. Yehova adzalanganso mitundu ina. Ngakhale Yerusalemu adzawonongeke, patsogolopo mzindawo udzakonzedwanso, ndipo anthu odzichepetsa ndi olungama adzakhala m'menemo.Za mkatimuZa tsiku la Yehova pamene Mulungu adzaimba mlandu 1.1—2.3Tsoka lodzagwera mitundu ina ya anthu yozungulira Israele 2.4-15Tsoka lodzagwera Yerusalemu; adzalapa ndipo Yehova adzamuwombola 3.1-20