2 AKORINTO 2 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 2Ako. 12.20-21 Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi chisoni.

2Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni?

32Ako. 7.16; 12.20-21Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse.

4Pakuti m'chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa.

5 1Ako. 5.1 Koma ngati wina wachititsa chisoni, sanachititsa chisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse.

61Tim. 5.20Kwa wotereyo chilango ichi chidachitika ndi ambiri chikwanira;

7Agal. 6.1kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.

8Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.

9Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse.

10Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso pa Khristu;

11kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake.

12Mac. 16.8; 1Ako. 16.9Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,

132Ako. 7.5-6ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya.

Makhalidwe ndi zipatso za utumiki wa Paulo

14Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.

151Ako. 1.18Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa;

16Yoh. 9.39; 2Ako. 3.5; 1Pet. 2.7-8koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?

172Ako. 4.2; 11.13Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help