1 2Mbi. 33.1-9 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba.
22Maf. 16.3Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.
31Maf. 16.32-33; 2Maf. 18.4Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.
41Maf. 8.29; Yer. 32.34Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, M'Yerusalemu ndidzaika dzina langa.
5Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.
62Maf. 17.17Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.
72Maf. 21.4Ndipo anaika chifanizo chosema chimene adachipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomoni mwana wake kuti, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israele ndidzaikamo dzina langa kosatha.
82Sam. 7.10Ndipo sindidzachotsanso mapazi a Israele m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; chokhachi asamalire kuchita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa chilamulo chonse anawalamulira Mose mtumiki wanga.
9Miy. 29.12Koma sanamvere, nawalakwitsa Manase, nawachititsa choipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israele.
10Pamenepo Yehova ananena mwa atumiki ake aneneri, ndi kuti,
112Maf. 23.26-27Popeza Manase mfumu ya Yuda anachita zonyansa izi, pakuti zoipa zake zinaposa zonse adazichita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ake;
12chifukwa chake atero Yehova Mulungu wa Israele, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda choipa, chakuti yense achimvera chidzamliritsa mwini khutu.
13Yes. 28.17Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.
14Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse;
15popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao m'Ejipito, mpaka lero lino.
162Maf. 24.3-4Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.
172Mbi. 33.11-19Machitidwe ena tsono a Manase, ndi zochimwa zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
18Nagona Manase ndi makolo ake, naikidwa m'munda wa nyumba yake, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwake Amoni mwana wake.
Amoni mfumu ya Yuda19 2Mbi. 33.21-25 Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.
202Maf. 21.2Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo amachitira Manase atate wake.
21Nayenda iye m'njira monse anayendamo atate wake, natumikira mafano anawatumikira atate wake, nawagwadira;
22nasiya Yehova Mulungu wa makolo ake, sanayende m'njira ya Yehova.
23Ndipo anyamata ake a Amoni anamchitira chiwembu, napha mfumuyo m'nyumba yakeyake.
24Koma anthu a m'dzikomo anapha onse akumchitira chiwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m'dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wake m'malo mwake.
25Machitidwe ena tsono a Amoni adawachita, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
26Naikidwa iye m'manda mwake m'munda wa Uza; nakhala mfumu m'malo mwake Yosiya mwana wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.