MASALIMO 43 - Buku Lopatulika Bible 2014

Davide alira akhale ku Kachisi

1 Mas. 35.1; 1Sam. 24.15 Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo.

Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.

2 Mas. 42.9 Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji?

Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?

3 Mas. 27.1 Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere;

zindifikitse kuphiri lanu loyera,

kumene mukhala Inuko.

4Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu,

kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni,

ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

5 Mas. 42.5, 11 Udziweramiranji moyo wanga iwe?

Ndi kuzingwa m'kati mwanga?

Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso,

ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help