MASALIMO 46 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu ndiye pothawirapo anthu akeKwa Mkulu wa Nyimbo; Chilangizo cha kwa ana a Kora. Pa Alamot. Nyimbo.

1 Mas. 91.2; Deut. 4.7 Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu,

thandizo lopezekeratu m'masautso.

2Chifukwa chake sitidzachita mantha,

lingakhale lisandulika dziko lapansi,

angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.

3 Yer. 5.22 Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu,

nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.

4 Chiv. 22.1-2 Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu.

Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.

5 Ezk. 43.7, 9; Yow. 2.27; Zek. 2.5 Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika,

Mulungu adzauthandiza mbandakucha.

6 Mas. 2.1 Amitundu anapokosera, maufumu anagwedezeka,

ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.

7 Num. 14.9 Yehova wa makamu ali ndi ife;

Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

8Idzani, penyani ntchito za Yehova,

amene achita zopululutsa pa dziko lapansi.

9 Yes. 2.4 Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;

athyola uta, nadula nthungo;

atentha magaleta ndi moto.

10 Eks. 14.13; Yes. 2.11, 17 Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu,

Ndidzabuka mwa amitundu,

ndidzabuka pa dziko lapansi.

11 Mas. 46.7 Yehova wa makamu ali ndi ife,

Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help