1Ndipo ananena nane, Wobadwa ndi munthu iwe, Idya chimene wachipeza; idya mpukutu uwu, numuke ndi kunena ndi nyumba ya Israele.
2Ezk. 2.8-9Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndipo anandidyetsa mpukutuwo.
3Yer. 15.16Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uchi.
4Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Muka, nufike kwa nyumba ya Israele, nunene nao mau anga.
5Pakuti sutumizidwa kwa anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, koma kwa nyumba ya Israele;
6Mat. 11.21, 23si kwa mitundu yambiri ya anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, amene sukhoza kudziwitsa chinenedwe chao. Zedi ndikakutumiza kwa iwowa adzamvera iwe.
7Yoh. 15.20Koma nyumba ya Israele siidzakumvera, pakuti siifuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israele ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.
8Taona ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zao; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yao.
9Ezk. 2.6Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
10Yer. 26.2-3Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.
11Numuke, nufike kwa andende kwa ana a anthu a mtundu wako, nunene nao ndi kuwauza, Atero Yehova Mulungu, ngakhale akamva kapena akaleka kumva.
12 Ezk. 8.3; 2Ako. 12.2-4 Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukulu, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwake.
13Ndipo ndinamva mkokomo wa mapiko a zamoyozo pakukhudzana, ndi mlikiti wa njingazo m'mbali mwa izo, ndilo phokoso la mkokomo waukulu.
14Ezk. 3.12M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.
15Ezk. 1.1Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako wodabwa pakati pao masiku asanu ndi awiri.
Mlonda wa Israele16Ndipo kunali atatha masiku asanu ndi awiri, mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,
17Yes. 52.8; 62.6; Yer. 6.17Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israele, m'mwemo mvera mau otuluka m'kamwa mwanga, nundichenjezere iwo.
18Yoh. 8.21, 24Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamchenjeza, wosanena kumchenjeza woipayo aleke njira yake yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.
19Mac. 20.26Koma ukachenjeza woipa, osabwerera iye kuleka choipa chake kapena njira yake yoipa, adzafa mu mphulupulu yake; koma iwe walanditsa moyo wako.
20Ezk. 18.24; 33.12-13Momwemonso akabwerera wolungama kuleka chilungamo chake, ndi kuchita chosalungama, ndipo ndikamuikira chomkhumudwitsa, adzafa; popeza sunamchenjeza, adzafa m'tchimo lake, ndi zolungama zake adazichita sizidzakumbukika; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.
21Koma ukamchenjeza wolungamayo, kuti asachimwe wolungamayo, ndipo sachimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anachenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako.
22Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, tuluka kunka kuchidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.
23Ezk. 1.1-28Ndipo ndinauka ndi kutuluka kunka kuchidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona kumtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.
24Ezk. 2.2Pamenepo unandilowa mzimu ndi kundiimika ndikhale chilili; ndipo analankhula ndi ine, nanena nane, Muka, katsekedwe m'nyumba mwako.
25Ezk. 4.8Koma iwe wobadwa ndi munthu, taona, adzakuikira iwe zingwe zolimba, nadzakumanga nazo, ndipo sudzatuluka pakati pao;
26Luk. 1.20-22ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
27Ezk. 3.11Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wosafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.