1Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi ntchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse zili m'tsogolo mwao.
2Mas. 73.3, 12-13Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira.
3Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
4Pakuti woyang'ana ndi amoyo onse ali nacho chiyembekezo; pakuti galu wamoyo aposa mkango wakufa.
5Yes. 26.14Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.
6Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kalikonse kachitidwe pansi pano.
7Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.
8Chiv. 3.4Zovala zako zikhale zoyera masiku onse; mutu wako usasowe mafuta.
9Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.
10Aro. 12.11Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Nzeru ya mwini ilanditsa ena11 Amo. 2.14-15; Yer. 9.23 Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe atamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.
12Luk. 12.20, 39; 1Ate. 5.3Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa m'ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
13Ndaonanso nzeru pansi pano motero, ndipo inandionekera yaikulu;
14panali mudzi waung'ono muli anthu owerengeka; ndipo inadzako mfumu yaikulu, niizinga ndi nkhondo, nimangapo malinga akulu;
15koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mudziwo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.
16Eks. 22.28; Miy. 21.22; Mac. 23.5Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.
17Mau a anzeru achete amveka koposa kufuula kwa wolamulira mwa zitsiru.
18Yos. 7.1, 11-12Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.