YESAYA 25 - Buku Lopatulika Bible 2014

Nyimbo yakulemekeza chifundo cha Mulungu

1 Eks. 5.2; Mas. 98.1 Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.

2Chifukwa Inu mwasandutsa mudzi muunda; mudzi walinga bwinja; nyumba ya alendo kuti isakhale mudzi; sudzamangidwa konse.

3Chiv. 11.13Chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mudzi wa mitundu yakuopsa udzakuopani Inu.

4Yes. 4.6Chifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba tchemba.

5Monga kutentha m'malo ouma, Inu mudzaletsa phokoso la alendo; nyimbo ya akuopsa idzaletseka, monga mthunzi uletsa dzuwa.

6Mat. 8.11Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.

7Aef. 4.18Ndipo Iye adzaononga m'phiri limeneli chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsalu yokuta amitundu onse.

81Ako. 15.54; Chiv. 7.17Iye wameza imfa kunthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.

9 Mas. 20.5; Tit. 2.13 Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.

10Chifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Mowabu adzaponderezedwa pansi m'malo ake, monga udzu aponderezedwa padzala.

11Ndipo iye adzatambasula manja ake pakati pamenepo, monga wosambira atambasula manja ake posambira; koma Iye adzagwetsa pansi kunyada kwake, pamodzi ndi kunyenga kwa manja ake.

12Ndipo linga la pamsanje la machemba ako Iye waligwetsa, naligonetsa pansi, nalifikitsa padothi, ngakhale pafumbi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help