1Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani.
2Mat. 24.43-44; 2Pet. 3.10Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.
3Yes. 13.6-9Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
4Aro. 6.19Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala;
5Aef. 5.8pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima;
6Mat. 25.1-13chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.
7Luk. 21.34-36Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku.
8Aef. 6.14-17Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.
92Ate. 2.13-14Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu,
10Aro. 14.8-9amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.
11Mwa ichi chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita.
Malangizo12 Afi. 2.29; 1Tim. 5.17 Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu;
13Mrk. 9.50ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.
14Akol. 3.12; 2Ate. 3.11-12Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima? Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
15Mat. 5.39, 44Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.
16Afi. 4.4Kondwerani nthawi zonse;
17Aef. 6.18Pempherani kosaleka;
18Akol. 3.17M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
19Aef. 4.30Musazime Mzimuyo;
201Ako. 14.1, 39Musanyoze manenero;
21Afi. 4.8; 1Yoh. 4.1Yesani zonse; sungani chokomacho,
22Mupewe maonekedwe onse a choipa.
23Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
241Ako. 1.9Wakuitana inu ali wokhulupirika, amenenso adzachichita.
25Akol. 4.3Abale, tipempherereni ife.
26Aro. 16.16Perekani moni kwa abale onse ndi chipsompsono chopatulika.
27Akol. 4.16Ndikulumbirirani pa Ambuye kuti kalatayu awerengedwe kwa abale onse.
28Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale nanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.