1 Eks. 25 Ndipo Bezalele anapanga likasa la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu;
2ndipo analikuta ndi golide woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wa golide pozungulira pake.
3Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide pa miyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake imodzi, ndi mphete ziwiri pa mbali yake ina.
4Ndipo anapanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide.
5Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa.
6Ndipo anapanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.
7Anapanganso akerubi awiri agolide; anachita kuwasula mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo;
8kerubi mmodzi pa mbali yake imodzi, ndi kerubi wina pa mbali yake ina; anapanga akerubi ochokera m'chotetezerapo, pa mathungo ake awiri.
9Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zopenyana; zinapenya kuchotetezerapo nkhope zao.
Gome la mkate woonekera10Ndipo anapanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu;
11ndipo analikuta ndi golide woona, nalipangira mkombero wagolide pozungulira pake.
12Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira anapangirapo mkombero wagolide.
13Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide, naika mphetezo pangodya zake zinai zokhala pa miyendo yake inai.
14Mphetezo zinali pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko kunyamulira nazo gomelo.
15Ndipo anapanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide, kunyamulira nazo gomelo.
16Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo, za golide woona.
Choikapo nyali17Ndipo anapanga choikapo nyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikapo nyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo;
18ndi m'mbali zake munatuluka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m'mbali yake imodzi, ndi mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m'mbali yake ina;
19pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyali.
20Ndipo pa choikapo nyali chomwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake;
21ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m'mwemo.
22Mitu yao ndi mphanda zao zinatuluka m'mwemo; chonsechi chinali chosulika pamodzi cha golide woona.
23Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona.
24Anachipanga ichi ndi zipangizo zake zonse za talente wa golide woona.
Guwa lofukizapo25Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wakasiya; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zinatuluka m'mwemo.
26Ndipo analikuta ndi golide woona, pamwamba pake, ndi mbali zake pozungulira, ndi nyanga zake; ndipo analipangira mkombero wagolide pozungulira pake.
27Ndipo analipangira mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake, pangodya zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo.
28Ndipo anazipanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide.
29Eks. 30.1-8, 23-38Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosanganiza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.