1 Aleluya.
Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera;
mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake.
2 Mas. 145.5-6 Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba;
mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji.
3Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga;
mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze.
4 Eks. 15.20; Yes. 38.20 Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe:
Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro.
5 1Mbi. 15—16; 19; 28 Mlemekezeni ndi nsanje zomveka:
Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa.
6 Mas. 145.21 Zonse zakupuma zilemekeze Yehova.
Aleluya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.