TITO 2 - Buku Lopatulika Bible 2014

Machenjezedwe a okalamba ndi anyamata ndi akapolo. Akhale chitsanzo yekha Tito

1Koma iwe, lankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa:

2Tit. 1.13okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro.

31Tim. 2.9-10Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;

41Tim. 5.14kuti akalangize akazi aang'ono akonde amuna ao, akonde ana ao,

5Aro. 2.24; Aef. 5.22akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.

6Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa;

7Aro. 3.20-22m'zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m'chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko,

81Pet. 2.12mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.

9Akol. 3.22Akapolo amvere ambuye ao a iwo okha, nawakondweretse m'zonse; osakana mau ao;

10Mat. 5.16osatapa pa zao, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse.

11Aro. 5.15Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse,

12Aro. 6.19ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;

13Afi. 3.20akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;

14Agal. 1.4; 1Pet. 2.9amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.

15 1Tim. 4.12 Izi lankhula, ndipo uchenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help