MASALIMO 7 - Buku Lopatulika Bible 2014

Adani amzinga, Davide adziponya kwa MulunguSyigayoni wa Davide woimbira Yehova, chifukwa cha mau a Kusi Mbenjamini.

1 Mas. 31.15 Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu;

mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;

2 Yes. 38.13 kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango,

ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.

3 1Sam. 24.11 Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita ichi;

ngati m'manja anga muli chosalungama;

4ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine;

(inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa);

5mdani alondole moyo wanga, naupeze;

naupondereze pansi moyo wanga,

naukhalitse ulemu wanga m'fumbi.

6 Mas. 94.2 Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,

nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa;

ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.

7Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu;

ndipo pamwamba pao mubwerere kunka kumwamba.

8 Mas. 18.20 Yehova aweruza anthu mlandu;

mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa,

ndi ungwiro wanga uli mwa ine.

9 1Sam. 16.7; Yer. 11.20; Chiv. 2.23 Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani,

koma wolungamayo mumkhazikitse.

Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.

10Chikopa changa chili ndi Mulungu,

wopulumutsa oongoka mtima.

11Mulungu ndiye Woweruza wolungama,

ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.

12Akapanda kutembenuka munthu,

iye adzanola lupanga lake;

wakoka uta wake, naupiringidza.

13Ndipo anamkonzera zida za imfa;

mivi yake aipanga ikhale yansakali.

14 Yak. 1.15 Taonani, ali m'chikuta cha zopanda pake;

anaima ndi chovuta, nabala bodza.

15 Est. 7.10; Mas. 9.15 Anachita dzenje, nalikumba,

nagwa m'mbuna yomwe anaikumba.

16 1Maf. 2.32 Chovuta chake chidzambwerera mwini,

ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.

17Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake;

ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help