1 Yes. 44.6 Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga.
2Mas. 66.12; Dan. 3.25, 27Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
3Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m'malo mwako.
4Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.
5Yes. 41.10Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo.
6Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kuchokera kutali, ndi ana anga akazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi;
7Yak. 2.7; 2Ako. 5.17-18; Aef. 2.10yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.
8Tulutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu.
9Yes. 41.21-22, 26
Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ichi ndi kuonetsa ife zinthu zakale? Atenge mboni zao, kuti avomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.10Yes. 41.4; 42.1; Yoh. 15.27Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.
11Hos. 13.4Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.
12Yes. 43.10Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.
13Yoh. 8.58Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa?
14Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao.
15Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israele, Mfumu yanu.
16Eks. 14.16, 22; Yos. 3.13, 16Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu;
17amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi.
18Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale.
19Eks. 17.6; Num. 20.11; 2Ako. 5.17; Chiv. 21.5Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala.
20Nyama za m'thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m'chipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;
21Aef. 1.5-6anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.
22Mik. 6.3; Mala. 1.13Komabe iwe sunandiitane Ine, Yakobo; koma iwe walema ndi Ine, Israele.
23Amo. 5.25Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritsa ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi lubani.
24Mala. 2.17Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndalama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi machimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.
25Yer. 31.34; 50.20; Ezk. 36.22-23; Mac. 3.19Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.
26Yes. 1.18Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe.
27Atate wako woyamba anachimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine.
28Yer. 24.9Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.