AFILIPI Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014

Mau Oyamba Kalata ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Afilipi inalembedwa ku mpingo woyamba umene Paulo anakhazikitsa ku Ulaya. Kalatayi inalembedwa pamene mtumwiyo anali m'ndende, ndipo pamene amavutitsidwa ndi akhristu ena amene amatsutsana ndi Paulo ndipo iye anakhumudwa chifukwa cha chiphunzitso chonyenga mu mpingo wa Filipi. Komabe mkalatayi muli chimwemwe ndi kutsimikizika mtima kumene kukupezeka chifukwa cha chikhulupiriro chozama mwa Yesu Khristu chimene Paulo anali nacho.Chifukwa choyambirira cholembera kalatayi chinali kuwathokoza akhristu a ku Filipi chifukwa cha mphatso imene iwo anatumiza kuti imuthandize panthawi imene iye anali kusowa. Tsono Pauloyo anagwiritsa ntchito mwayiwu pofuna kuwatsimikizira kuti iwo alimbike mtima ndi kuchilimika ngakhale iye anali pa mavuto amene anali mavuto awonso. Iye akuwadandaulira kuti akhale ndi mtima wodzichepetsa ngati wa Yesu, m'malo mokhala moyo wodzikonda ndi wodzitukumula. Iye akuwakumbutsa kuti umodzi wao ndi Khristu ndi mphatso ya chisomo cha Mulungu chimene iwo analandira mwa chikhulupiriro, osati kudzera mu kumvera miyambo ya malamulo a Chiyuda. Iye akulemba za chimwemwe ndi mtendere zimene Mulungu amapereka kwa iwo amene amakhala moyanjana ndi Khristu.Kalatayi imadziwika bwino chifukwa cha kutsindika pa mfundo ya chimwemwe, kudzidalira, umodzi, kupirira pa moyo wa Chikhristu. Ikuonetsanso chikondi chimene Paulo anali nacho pa mpingo wa ku Filipi.Za mkatimuMau oyamba 1.1-11Zimene Paulo anakumana nazo 1.12-26Moyo mwa Khristu 1.27—2.18Chikonzero cha Paulo pa Timoteo ndi Epafrodito 2.19-30Machenjezo pa adani komanso zoopsa 3.1—4.9Paulo ndi anzake a ku Filipi 4.10-20Mau omaliza 4.21-23
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help