1Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao,
2Mac. 10.14; Aheb. 9.10Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili pa dziko lapansi.
3Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.
4Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda; ngamira, angakhale abzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa.
5Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika chiboda, muiyese yodetsedwa.
6Ndi kalulu, popeza abzikula koma wosagawanika chiboda, mumuyese wodetsedwa.
7Ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.
8Nyama yake musamaidya, mitembo yake musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.
9Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya.
10Koma zilizonse zilibe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse zili m'madzi, muziziyesa zonyansa;
11inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.
12Zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba m'madzimo muziyese zonyansa.
13Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; siziyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi;
14ndi muimba, ndi mphamba mwa mtundu wake;
15khungubwi mwa mtundu wake;
16ndi nthiwatiwa, ndi chipudo, ndi kakowa, ndi kabawi mwa mtundu wake;
17ndi nkhutukutu ndi nswankhono ndi manchichi;
18tsekwe, vuwo, ndi dembo;
19indwa, ndi chimeza monga mwa mtundu wake, ndi sadzu, ndi mleme.
20Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa.
21Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kuthumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi:
22dzombe mwa mtundu wake, ndi chirimamine mwa mitundu yake, ndi njenjete mwa mtundu wake ndi tsokonombwe mwa mitundu yake.
23Koma zokwawa zonse zakuuluka, za miyendo inai, muziyese zonyansa.
24Ndipo izi zikudetsani: aliyense akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;
25ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
26Nyama iliyonse yakugawanika chiboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; aliyense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.
27Ndipo iliyonse iyenda yopanda chiboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; aliyense wokhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
28Ndipo iye amene akanyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.
29Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wake;
30ndi gondwa, ndi mng'azi, ndi buluzi, ndi dududu, ndi birimankhwe.
31Izi ndi zimene muziyese zodetsa, mwa zonse zakukwawa; aliyense azikhudza zitafa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
32Ndipo chilichonse chakufa cha izi chikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale chipangizo chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa kapena thumba, chipangizo chilichonse chimene agwira nacho ntchito, achiviike m'madzi, ndipo chidzakhala chodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo chidzakhala choyera.
33Ndipo chilichonse cha izi chikagwa m'chotengera chilichonse chadothi, chinthu chokhala m'mwemo chidetsedwa, ndi chotengeracho muchiswe.
34Chakudya chilichonse chokhala m'mwemo, chokonzeka ndi madzi, chidzakhala chodetsedwa; ndi chakumwa chilichonse m'chotengera chotere chidzakhala chodetsedwa.
35Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa zinthu zilizonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mchembo kapena mphika wovundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa.
36Koma kasupe kapena chitsime muli madzi, zidzakhala zoyera; koma iye amene akhudza mitembo yao adzadetsedwa.
37Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa mbeu yofesa, ikati ifesedwe, idzakhala yoyera.
38Koma akathira madzi pa mbeuyi, ndi kanthu ka mtembo wake kakagwapo, muiyese yodetsedwa.
39Ndipo ikafa nyama yakudya, iye amene akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
40Ndipo iye wakudya kanthu ka mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; iyenso wakunyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
41Ndipo zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi zikhale zonyansa; musamazidya.
42Zonse zoyenda chafufumimba, ndi zonse za miyendo inai, kapena zonse zokhala nayo miyendo yambiri ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, musamazidya; popeza ndizo zonyansa.
43Musamadzinyansitsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa, musamadzidetsa nazo, kuti mukadziipse nazo.
44Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa pansi.
45Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera.
46Ichi ndi chilamulo cha nyama, ndi cha mbalame, ndi cha zamoyo zonse zakuyenda m'madzi, ndi cha zamoyo zonse zakukwawa pansi;
47kusiyanitsa pakati zodetsa ndi zoyera, ndi pakati pa zamoyo zakudya ndi zamoyo zosadya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.