YESAYA 15 - Buku Lopatulika Bible 2014

Aneneratu za kuonongeka kwa Mowabu

1 Yer. 48 Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe.

2Deut. 34.1; Ezk. 7.18Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.

3M'makwalala mwao adzimangira chiguduli m'chuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.

4Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake.

5Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.

6Pakuti pa madzi a Nimurimu padzakhala mabwinja; popeza udzu wafota, msipu watha.

7Chifukwa chake zochuluka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo kumtsinje wa mabango.

8Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu.

92Maf. 17.25Pakuti madzi a Diboni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa Diboni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Mowabu, ndi pa otsala a m'dziko.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help