1Koma kuli mtapo wa siliva,
ndi malo a golide amene amuyenga.
2Chitsulo achitenga m'nthaka,
ndi mkuwa ausungunula kumwala.
3Munthu athawitsa mdima,
nafunafuna mpaka malekezero onse,
miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.
4Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu;
aiwalika ndi phazi lopitapo;
apachikika kutali ndi anthu, nalendewalendewa.
5Kunena za nthaka, kuchokera momwemo mumatuluka chakudya,
ndi m'munsi mwake musandulizika ngati ndi moto.
6Miyala yake ndiyo malo a safiro,
ndipo ili nalo fumbi lagolide.
7Njira imeneyi palibe chiombankhanga chiidziwa;
lingakhale diso la kabawi losapenyapo.
8Nyama zodzikuza sizinapondapo,
ngakhale mkango waukali sunapitapo.
9Munthu atambasulira dzanja lake kumwala;
agubuduza mapiri kuyambira kumizu.
10Asema njira pakati pa matanthwe,
ndi diso lake liona chilichonse cha mtengo wake.
11Atseka mitsinje ingadonthe;
natulutsira poyera chobisikachi.
12Koma nzeru, idzapezeka kuti?
Ndi luntha, malo ake ali kuti?
13 Miy. 3.15 Munthu sadziwa mtengo wake;
ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.
14Pozama pakuti, Mwa ine mulibe;
ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe.
15 Miy. 3.15 Silipezeka ndi golide,
sayesapo siliva mtengo wake.
16Sailinganiza ndi golide wa Ofiri,
ndi sohamu wa mtengo wake wapatali kapena safiro.
17Golide ndi krustalo sizilingana nayo;
ndi kusinthana kwake,
siisinthanika ndi zisambiro za golide woyengetsa.
18Korali kapena ngale sizikumbukikapo.
Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira.
19Topazi wa Kusi sufanana nayo,
sailinganiza ndi golide wolongosoka.
20Koma nzeru ifuma kuti?
Ndi luntha, pokhala pake pali kuti?
21Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,
pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga.
22Chionongeko ndi Imfa zikuti,
Tamva mbiri yake m'makutu mwathu.
23Mulungu ndiye azindikira njira yake,
ndiye adziwa pokhala pake.
24 Miy. 15.3 Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi,
naona pansi pa thambo ponse;
25pamene anaikira mphepo muyeso wake,
nayesera madzi miyeso;
26pakuchitira mvula lamulo,
ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;
27pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera;
anaikonza, naisanthula.
28 Mas. 111.10; Miy. 1.7 Koma kwa munthu anati,
Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru;
ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.