LEVITIKO 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Aroni adziperekera yekha ndi anthu nsembe, ndizo nsembe zoyamba

1Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chitatu, kuti Mose anaitana Aroni ndi ana ake amuna, ndi akulu a Israele;

2ndipo anati kwa Aroni, Dzitengere mwanawang'ombe wamwamuna, akhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopsereza, zopanda chilema, nubwere nazo pamaso pa Yehova.

3Nunene kwa ana a Israele, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yauchimo; ndi mwanawang'ombe, ndi mwanawankhosa, a chaka chimodzi, opanda chilema, akhale nsembe yopsereza;

4ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosanganiza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.

5Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pa chihema chokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova.

6Ndipo Mose anati, Ichi ndi chimene Yehova anakuuzani kuti muchichite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu.

7Aheb. 5.1-3Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yauchimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzichitire wekha ndi anthuwo chotetezera; nupereke chopereka cha anthu, ndi kuwachitira chotetezera; monga Yehova anauza.

8Pamenepo Aroni anasendera kufupi kwa guwa la nsembe, napha mwanawang'ombe wa nsembe yauchimo, ndiyo ya kwa iye yekha.

9Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde pa guwa la nsembe;

10koma mafutawo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa za nsembe yauchimo, anazitentha pa guwa la nsembe; monga Yehova anauza Mose.

11Ndipo anatentha ndi moto nyamayi ndi chikopa kunja kwa chigono.

12Ndipo anapha nsembe yopsereza; ndi ana a Aroni anapereka mwaziwo kwa iye, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira.

13Ndipo anapereka nsembe yopsereza kwa iye, chiwalochiwalo, ndi mutu wake; ndipo anazitentha pa guwa la nsembe.

14Ndipo anatsuka matumbo ndi miyendo, nazitentha pa nsembe yopsereza pa guwa la nsembe.

15Ndipo anabwera nacho chopereka cha anthu, natenga mbuzi ya nsembe yauchimo ndiyo ya kwa anthu, naipha, naipereka nsembe yauchimo, monga yoyamba ija.

16Ndipo anabwera nayo nsembe yopsereza naipereka monga mwa lemba lake.

17Ndipo anabwera nayo nsembe yaufa, natengako wodzala dzanja, nautentha pa guwa la nsembe, angakhale adatentha nsembe yopsereza ya m'mawa.

18Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira,

19ndi mafuta a ng'ombe; ndi a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira wamafuta, ndi chophimba matumbo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa;

20ndipo anaika mafuta pa ngangazo, natentha mafutawo pa guwa la nsembe.

21Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga Iye anauza Mose.

22Luk. 24.50Ndipo Aroni anakweza dzanja lake kulozera anthu, nawadalitsa; natsika kuja anapereka nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika.

23Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku chihema chokomanako, natuluka, nadalitsa anthu; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.

241Maf. 18.38-39; 2Mbi. 7.1Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta pa guwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help