NEHEMIYA Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014
Mau OyambaBuku la Nehemiya tingathe kuligawa mu magawo anai: Gawo loyamba ndi pamene Nehemiya akubwerera ku Yerusalemu, atatumizidwa ndi mfumu ya ku Persiya kuti akakhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda. Gawo lachiwiri ndi pamene akumanganso malinga a Yerusalemu. Lachitatu ndi pamene Ezara akuwerenga Malamulo a Mulungu anthuwo nalapa machimo. Gawo lachinai ndi ntchito zina zimene Nehemiya anazichita pokhala bwanamkubwa wa ku Yuda.Chinthu chodziwika bwino mu bukuli ndi mbiri ya moyo wa Nehemiya wodalira pa Mulungu komanso kukonda kupemphera.Za mkatimuNehemiya abwerera ku Yerusalemu 1.1—2.20Kumangidwanso kwa makoma a Yerusalemu 3.1—7.73Lamulo liwerengedwa, ndipo anthu akonzanso mapangano ao 8.1—10.39Ntchito zina za Nehemiya 11.1—13.31