1 1Maf. 10.1-13 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndi ngamira zosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.
2Ndipo Solomoni anammasulira mau ake onse, panalibe kanthu kombisikira Solomoni, kamene sanammasulire.
3Ndipo mfumu yaikazi ya ku Sheba ataiona nzeru ya Solomoni, ndi nyumba adaimanga,
4ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi mavalidwe ao, ndi makweredwe ake pokwera iye kunka kunyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.
5Ndipo anati kwa mfumu, Inali yoona mbiri ija ndidaimva m'dziko langa, ya machitidwe anu, ndi ya nzeru zanu.
6Koma sindinakhulupirira mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zochuluka; mwaonjezatu pa mbiri ndidaimva.
7Odala anthu anu, ndi odala anyamata anu awa akuima chiimirire pamaso panu, ndi kumva nzeru zanu.
8Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Aisraele kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kuchita chiweruzo ndi chilungamo.
9Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wake; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Sheba anapatsa mfumu Solomoni.
102Mbi. 8.18Ndiponso anyamata a Huramu, ndi anyamata a Solomoni otenga golide ku Ofiri, anatenga mitengo yambawa ndi timiyala ta mtengo wapatali.
11Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oimbira; sizinaoneka zotere ndi kale lonse m'dziko la Yuda.
12Ndipo mfumu Solomoni anampatsa mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lake, iyeyu ndi anyamata ake.
Chuma ndi ulemerero wa Solomoni13 1Maf. 10.14-28 Kulemera kwake tsono kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi ndiko matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide;
14osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golide ndi siliva kwa Solomoni.
15Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri za golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera golide wonsansantha masekeli mazana awiri.
16Napanganso malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera masekeli mazana atatu a golide; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.
17Mfumu inapanganso mpando wachifumu waukulu wa minyanga, naukuta ndi golide woona.
18Ndi mpando wachifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi chopondapo mapazi chagolide, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo.
19Ndi mikango khumi ndi iwiri inaimirirapo, mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi; sanapangidwe wotere m'ufumu uliwonse.
20Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zipangizo zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali za golide woona; siliva sanayesedwe kanthu m'masiku a Solomoni.
21Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golide, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.
22Momwemo mfumu Solomoni inaposa mafumu onse a pa dziko lapansi, kunena za chuma ndi nzeru.
23Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake Mulungu adazilonga m'mtima mwake.
24Nabwera nao munthu yense mtulo wake, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolide, zovala, ndi zida za nkhondo, ndi mure, akavalo ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.
25Ndipo Solomoni anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magaleta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magaleta, ndi m'Yerusalemu kwa mfumu.
26Gen. 15.18; Mas. 72.8Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Ejipito.
27Ndipo mfumu inachulukitsa siliva m'Yerusalemu ngati miyala; ndi mikungudza anailinganiza ndi mikuyu ili kumadambo kuchuluka kwake.
28Ndipo anakamtengera Solomoni akavalo ku Ejipito, ndi ku maiko onse.
Kumwalira kwa Solomoni29Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwa kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati?
301Maf. 11.42-43Ndipo Solomoni anakhala mfumu ya Israele yense m'Yerusalemu zaka makumi anai.
31Nagona Solomoni pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.