ESTERE 5 - Buku Lopatulika Bible 2014

Estere alowa kwa mfumu nampempha iye ndi Hamani azidya naye

1 Est. 4.16 Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba.

2Est. 4.11; 8.4Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuluyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide inali m'dzanja lake. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.

3Mrk. 6.23Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkulu? Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

4Ndipo Estere anati, Chikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera.

5Niti mfumu, Mumfulumize Hamani, achitike mau a Estere. Nidza mfumu ndi Hamani ku madyerero adawakonzera Estere.

6Est. 9.12Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

7Nayankha Estere, nati, Pempho langa ndi kufuna kwanga ndiko,

8ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso chakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kuchita chofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzachita monga yanena mfumu.

Hamani amangitsa popachika Mordekai

9 Est. 3.5 Ndipo Hamani anatuluka tsiku lomwelo wosekerera ndi wokondwera mtima; koma pamene Hamani anapenya Mordekai kuchipata cha mfumu, osamnyamukira kapena kumfumukira, Hamani anadzazidwa ndi mkwiyo pa Mordekai.

10Koma Hamani anadziletsa, namuka kwao, natumiza munthu kukatenga mabwenzi ake, ndi Zeresi mkazi wake.

11Est. 9.7-10Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.

12Hamani anatinso, Ndiponso Estere mkazi wamkulu sanalole mmodzi yense alowe pamodzi ndi mfumu ku madyerero adakonzawo, koma ine ndekha; nandiitana mawanso pamodzi ndi mfumu.

13Koma zonsezi sindipindula nazo kanthu konse, pokhala ndilikuona Mordekai Myudayo alikukhala kuchipata cha mfumu.

14Est. 7.9-10Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help