YOBU 19 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yobu atchulira mabwenzi ake matsoka ake, napempha amchitire chifundo. Adzitonthoza ndi Mpulumutsi wake

1Koma Yobu anayankha, nati,

2Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti,

ndi kundithyolathyola nao mau?

3 Gen. 3.7; 31.7 Kakhumi aka mwandichititsa manyazi;

mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.

4Ndipo ngati ndalakwa ndithu,

kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.

5Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,

ndi kunditchulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao.

6Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,

nandizinga ndi ukonde wake.

7Taonani, ndifuula kuti, Chiwawa! Koma sandimvera;

ndikuwa, koma palibe chiweruzo.

8Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,

naika mdima poyendapo ine.

9Anandivula ulemerero wanga,

nandichotsera korona pamutu panga.

10Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu;

nachizula chiyembekezo changa ngati mtengo.

11Wandiyatsiranso mkwiyo wake,

nandiyesera ngati wina wa adani ake.

12Ankhondo ake andidzera pamodzi, nandiundira njira yao,

nandimangira misasa pozinga hema wanga.

13 Mas. 31.11 Iye anandichotsera abale anga kutali,

ndi odziwana nane andiyesa mlendo konse.

14Anansi anga andisowa,

ndi odziwana nane bwino andiiwala.

15Iwo a m'nyumba mwanga ndi adzakazi anga andiyesa mlendo;

ndine wachilendo pamaso pao.

16Ndikaitana kapolo wanga, sandibwezera mau,

chinkana ndimpembedza pakamwa panga.

17Mpweya wanga unyansira mkazi wanga,

chinkana ndinampembedza ndi kutchula ana a thupi langa.

18 2Maf. 2.23 Angakhale ana ang'ono andipeputsa,

ndikanyamuka, andinena;

19 Mas. 41.9 mabwenzi anga enieni onse anyansidwa nane;

ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga.

20 Mas. 102.5 Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga,

ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga.

21 Mas. 38.2 Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu;

pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.

22 Mas. 69.26 Mundilondola bwanji ngati Mulungu,

losakukwanirani thupi langa?

23Ha! Akadalembedwa mau anga!

Ha! Akadalembedwa m'buku!

24Akadawazokota pathanthwe chikhalire,

ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu!

25Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo,

nadzauka potsiriza pafumbi.

26 Mas. 17.15; 1Ako. 13.12; 1Yoh. 3.2 Ndipo khungu langa litaonongeka,

pamenepo wopanda thupi langa, ndidzapenya Mulungu,

27amene ndidzampenya ndekha,

ndi maso anga adzamuona, si wina ai.

Imso zanga zatha m'kati mwanga.

28Mukati, Tiyeni timlondole!

Popeza chifukwa cha mlandu chapezeka mwa ine;

29 Mas. 58.10-11 muchite nalo mantha lupanga;

pakuti mkwiyo utenga zolakwa za lupanga,

kuti mudziwe pali chiweruzo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help