YOBU 42 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yobu adzichepetsa pamaso pa Mulungu, mabwenziwo adzudzulidwa ndi Mulungu, Yobu apulumutsidwa nadalitsidwanso

1Pamenepo Yobu anayankha Yehova, nati,

2 Gen. 18.14; Mat. 19.26 Ndidziwa kuti mukhoza kuchita zonse,

ndi kuti palibe choletsa cholingirira chanu chilichonse.

3 Mas. 40.5 Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu?

Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikira,

zondidabwitsa, zosazidziwa ine.

4Tamveranitu, ndidzanena ine,

ndidzakufunsani, mundidziwitse.

5Kumva ndidamva mbiri yanu,

koma tsopano ndikupenyani maso;

6 Ezr. 9.6; Yob. 40.4 chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa

m'fumbi ndi mapulusa.

7Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.

8Gen. 20.7, 17; Mat. 5.24; Yak. 5.15-16; 1Yoh. 5.16Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki Yobu.

9Namuka Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, nachita monga Yehova adawauza; ndipo Yehova anavomereza Yobu.

10 Mas. 14.7; Yes. 61.7 Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.

11Pamenepo anamdzera abale ake onse, ndi alongo ake onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m'nyumba yake, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndalama ndi mphete yagolide.

12Yob. 1.3; Yak. 5.11Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake, ndipo anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinai, ndi ngamira zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng'ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu akazi chikwi chimodzi.

13Anali naonso ana amuna asanu ndi awiri ndi ana akazi atatu.

14Ndipo anamutcha dzina la woyamba Yemima, ndi dzina la wachiwiri Keziya, ndi dzina la wachitatu Kerenihapuki.

15Ndipo m'dziko monse simunapezeka akazi okongola ngati ana akazi a Yobu, nawapatsa cholowa atate wao pamodzi ndi alongo ao.

16Miy. 3.16Ndipo zitatha izi, Yobu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi mphambu makumi anai, naona ana ake ndi zidzukulu zake mibadwo inai.

17Gen. 25.8Namwalira Yobu, wokalamba ndi wa masiku ochuluka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help