YOBU 23 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yobu abwereza kukana kuti sanachimwe. Mulungu wosadziwika achita chifuniro chake. Kwambiri ochimwa oyenera kulangidwa akhala bwino m'moyo uno

1Koma Yobu anayankha, nati,

2 Gen. 4.13 Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa;

kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwake.

3 2Mbi. 11.16 Ha! Ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu,

kuti ndifike kumpando wake!

4Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pake,

ndikadadzaza m'kamwa mwanga ndi matsutsano.

5Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine,

ndikadazindikira chimene akadanena nane.

6Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yake yaikulu?

Iai, koma akadanditcherera khutu.

7Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;

ndipo ndikadapulumuka chipulumukire kwa Woweruza wanga.

8Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye;

kapena m'mbuyo sindimzindikira;

9akachita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;

akabisala kulamanja, sindimuona.

10 Mas. 139.1-3, 24; Yak. 1.12 Koma adziwa njira ndilowayi;

atandiyesa ndidzatuluka ngati golide.

11 Mas. 44.18 Phazi langa lagwiratu moponda Iye,

ndasunga njira yake, wosapatukamo.

12 Yoh. 4.32, 34 Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake;

ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.

13Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani?

Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.

14 1Ate. 3.3 Pakuti adzachita chondiikidwiratu;

ndipo zambiri zotere zili ndi Iye.

15Chifukwa chake ndiopsedwa pankhope pake;

ndikalingirira, ndichita mantha ndi Iye.

16 Mas. 22.14 Pakuti Mulungu walefula mtima wanga,

ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.

17Popeza sindinalikhidwa usanafike mdimawo,

ndipo sanandiphimbire nkhope yanga ndi mdima wa bii.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help