1Ndipo gawo la ana a Yosefe linatuluka kuchokera ku Yordani ku Yeriko, ku madzi a Yeriko kum'mawa, kuchipululu, nakwera kuchokera ku Yeriko kunka kumapiri ku Betele;
2natuluka ku Betele kunka ku Luzi, napitirira kunka ku malire a Aariki, ku Ataroti;
3natsikira kumadzulo kunka ku malire a Ayafileti, ku malire a Betehoroni wa kunsi, ndi ku Gezere; ndi matulukiro ake anali kunyanja.
4Motero ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu analandira cholowa chao,
5Ndipo malire a ana a Efuremu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a cholowa chao kum'mawa ndiwo Ataroti-Adara, mpaka Betehoroni wa kumtunda;
6natuluka malire kumadzulo ku Mikametati kumpoto; nazungulira malire kum'mawa kunka ku Taanatisilo, naupitirira kum'mawa kwake kwa Yanowa:
7natsika kuchokera ku Yanowa, kunka ku Ataroti, ndi ku Naara, nafika ku Yeriko, natuluka ku Yordani.
8Kuyambira ku Tapuwa malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi matulukiro ake anali kunyanja. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuremu monga mwa mabanja ao;
9pamodzi ndi midzi adaipatulira ana a Efuremu pakati pa cholowa cha ana a Manase, midzi yonse pamodzi ndi milaga yao.
101Maf. 9.16Ndipo sanaingitse Akanani akukhala m'Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.