1Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m'chihema chokomanako Iye, nati,
2Lankhula ndi ana a Israele, nunene nao, Aliyense mwa inu akabwera nacho chopereka cha kwa Yehova, muzibwera nacho chopereka chanu chikhale cha zoweta, cha ng'ombe, kapena cha nkhosa, kapena cha mbuzi.
3Eks. 12.5Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.
4Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.
5Aheb. 12.24; 1Pet. 1.2Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako.
6Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zake.
7Ndipo ana a Aroni wansembeyo asonkhe moto pa guwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pamotopo;
8ndi ana a Aroni, ansembewo, akonze ziwalozo, mutu, ndi mafuta pa nkhuni zili pa moto wa pa guwa la nsembe;
9koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
10Ndipo chopereka chake chikakhala cha nkhosa, kapena cha mbuzi, chikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda chilema.
11Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira.
12Ndipo aikadzule ziwalo zake, pamodzi ndi mutu wake ndi mafuta ake; ndi wansembeyo akonze izi pa nkhuni zili pa moto wa pa guwa la nsembe.
13Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
14Ndipo chopereka chake cha kwa Yehova chikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera nacho chopereka chake chikhale cha njiwa, kapena cha maunda.
15Ndipo wansembe abwere nacho ku guwa la nsembe, namwetule mutu wake, naitenthe pa guwa la nsembe; ndi mwazi wake aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,
16nachotse chitsokomero, ndi chipwidza chake, nazitaye kufupi kwa guwa la nsembe, kum'mawa, kudzala;
17nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe pa guwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.