MLALIKI 11 - Buku Lopatulika Bible 2014

Tizichita zokoma lero lino posadziwa za mawa

1 Deut. 15.10; Yes. 32.20; Mat. 10.42 Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.

2Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa choipa chanji chidzaoneka pansi pano.

3Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwera pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo.

4Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.

5Mas. 139.14-15Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.

6Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.

7Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa.

8Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzachuluka. Zonse zilinkudza zili zachabe.

Anyamata asangalale, koma adzikonzeretu pokumbukira imfa ikudza

9 Aro. 2.6-11 Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.

102Ako. 7.1Chifukwa chake chotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa chabe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help