EKSODO 1 - Buku Lopatulika Bible 2014

Masautso a ana a Israele m'Ejipito

1 Gen. 46.8 Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa m'Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:

2Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda;

3Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini;

4Dani ndi Nafutali, Gadi ndi Asere.

5Gen. 46.27Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali m'Ejipito.

6Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse.

7Deut. 26.5; Mac. 7.17Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.

8Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Ejipito, imene siinadziwa Yosefe.

9Mas. 105.24Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu.

10Mac. 7.19Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo.

11Gen. 15.13; 47.11Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.

12Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.

13Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa;

14nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.

Anamwino samvera mfumu

15Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa;

16ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.

17Miy. 16.6Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana amuna akhale ndi moyo.

18Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana amunawo akhale ndi moyo?

19Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.

20Yes. 3.10Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu.

21Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anaopa Mulungu, Iye anawamangitsira mabanja.

22Mac. 7.19Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana amuna onse akabadwa aponyeni m'nyanja, koma ana akazi onse alekeni amoyo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help