1 1Maf. 6; 1Mbi. 21.18 Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.
2Nayamba kumanga tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri, chaka chachinai cha ufumu wake.
3Ndipo maziko adawaika Solomoni akumangapo nyumba ya Mulungu ndi awa: utali wake, kuyesa mikono monga mwa muyeso wakale, ndiwo mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.
4Ndi chipinda cholowera chinali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake zana limodzi mphambu makumi awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golide woona.
5M'nyumba yaikulu tsono anatchinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golide wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo.
6Ndipo anakuta nyumba ndi miyala ya mtengo wake; ndi golide wake ndiye golide wa Paravaimu.
7Anamamatizanso Kachisi, mitanda, ziundo, ndi makoma ake, ndi zitseko zake, ndi golide; nalemba akerubi pamakoma.
8Ndipo anamanga malo opatulika kwambiri, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; naikuta ndi golide wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi.
9Ndi kulemera kwake kwa misomali ndiko masekeli makumi asanu a golide. Ndipo anazikuta ndi golide zipinda zosanjikizana.
10Ndipo m'malo opatulika kwambiri anapanga akerubi awiri, anachita osema, nawakuta ndi golide.
11Ndi mapiko a akerubi m'litali mwake ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzake mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.
12Ndi phiko la kerubi wina mikono isanu lojima khoma la nyumba, ndi phiko linzake mikono isanu lolumikizana ndi phiko la kerubi wina.
13Mapiko a akerubi awa anafunyululika mikono makumi awiri; ndipo anaima ndi mapazi ao, ndi nkhope zao zinaloza kukhomo.
14Eks. 26.31; Mat. 27.51; Aheb. 9.3Ndipo anaomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiira, ndi lofiirira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, naomberamo akerubi.
151Maf. 7.15-21Ndipo anapanga ku khomo la nyumba nsanamira ziwiri za mikono makumi atatu mphambu ziwiri; ndi mutu unakhala pamwamba pa iliyonse ndiwo mikono isanu.
16Napanga maunyolo a m'chipinda chamkati, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo.
17Ndipo anaimiritsa nsanamirazo pakhomo pa Kachisi; imodzi ku dzanja lamanja, ndi inzake ku dzanja lamanzere; nalitcha dzina la iyi ya ku dzanja lamanja Yakini, ndi dzina la iyi ya ku dzanja lamanzere Bowazi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.