1 1Mbi. 16.8, 34 Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino;
pakuti chifundo chake nchosatha.
2 Mas. 115.9, 11 Anene tsono Israele,
kuti chifundo chake nchosatha.
3Anene tsono nyumba ya Aroni,
kuti chifundo chake nchosatha.
4Anene tsono iwo akuopa Yehova,
kuti chifundo chake nchosatha.
5 Mas. 56.13 M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;
anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.
6 Yes. 51.12; Aheb. 13.6 Yehova ndi wanga; sindidzaopa;
adzandichitanji munthu?
7 Mas. 54.4 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;
m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.
8 Yer. 17.5, 7 Kuthawira kwa Yehova nkokoma
koposa kukhulupirira munthu.
9 Mas. 146.3 Kuthawira kwa Yehova nkokoma
koposa kukhulupirira akulu.
10 Amitundu onse adandizinga,
zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
11Adandizinga, inde, adandizinga:
Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
12 Deut. 1.44 Adandizinga ngati njuchi;
anazima ngati moto waminga;
indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
13Kundikankha anandikankha ndikadagwa;
koma Yehova anandithandiza.
14 Yes. 12.2 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
ndipo anakhala chipulumutso changa.
15M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera
Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
16Dzanja lamanja la Yehova likwezeka,
Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu.
17 Hab. 1.12 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo,
ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.
18 2Ako. 6.9 Kulanga anandilangadi Yehova:
koma sanandipereke kuimfa ai.
19 Yes. 26.2 Nditsegulireni zipata za chilungamo;
ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.
20Chipata cha Yehova ndi ichi;
olungama adzalowamo.
21 Mas. 116.1 Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,
ndipo munakhala chipulumutso changa.
22 Mat. 21.42; Mrk. 12.10; Luk. 20.17; Mac. 4.11; Aef. 2.20 Mwala umene omangawo anaukana
wakhala mutu wa pangodya.
23Ichi chidzera kwa Yehova;
nchodabwitsa ichi pamaso pathu.
24Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;
tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.
25Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;
tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.
26 Mat. 21.9; 23.39 Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova;
takudalitsani kochokera m'nyumba ya Yehova.
27Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;
mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.
28 Yes. 25.1 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;
ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.
29 Mas. 118.1 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino,
pakuti chifundo chake nchosatha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.