1 Ezk. 40.3 Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo, ndi kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.
2Ezk. 40.17-20; Luk. 21.24Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.
3Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.
4Zek. 4.3, 11, 14Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikapo nyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.
5Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto utuluka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero.
6Eks. 7.19; Yak. 5.16-17Izo zili nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a chinenero chao; ndipo ulamuliro zili nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uliwonse nthawi iliyonse zikafuna.
7Chiv. 13.1Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chilombo chokwera kutuluka m'chiphompho chakuya chidzachita nazo nkhondo, nichidzazilaka, nichidzazipha izo.
8Aheb. 13.12; Chiv. 14.8Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala lamudzi waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, Sodomu ndi Ejipito, pameneponso Ambuye wao anapachikidwa.
9Mas. 79.2-3Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lake, osalola mitembo yao iikidwe m'manda.
10Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko.
11Ezk. 37.5-14Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chilili; ndipo mantha akulu anawagwera iwo akuwapenya.
12Ndipo anamva mau akulu akuchokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kunka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.
13Chiv. 6.12; 16.19Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mudzi lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m'Mwamba.
14 Chiv. 9.12 Tsoka lachiwiri lachoka; taonani, tsoka lachitatu lidza msanga.
Lipenga lotsiriza15 Chiv. 12.10 Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau akulu m'Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.
16Chiv. 4.4, 10Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yachifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu,
17Chiv. 1.4, 8nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.
18Dan. 7.9-10Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko.
19 Chiv. 15.5-8 Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali m'Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, m'Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala akulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.