YOBU 3 - Buku Lopatulika Bible 2014

Madandaulo a Yobu

1Atatero, Yobu anatsegula pakamwa pake, natemberera tsiku lake.

2Nalankhula Yobu nati,

3

9Nyenyezi za chizirezire zide;

uyembekezere kuunika, koma kuusowe;

usaone kephenyuka kwa mbandakucha;

10popeza sunatseka pa makomo ake mimba ya mai wanga.

Kapena kundibisira mavuto pamaso panga.

11Ndinalekeranji kufera m'mimba?

Ndi kupereka mzimu wanga pobadwa ine.

12Anandilandiriranji maondo?

Kapena mawere kuti ndiyamwe?

13Pakuti ndikadagona pansi pomwepo ndi kukhala chete;

ndikanagona tulo; pamenepo ndikadaona popumula;

14pamodzi ndi mafumu ndi maphungu a padziko,

akudzimangira m'mabwinja;

15kapena pamodzi ndi akalonga eni ake a golide,

odzaza nyumba zao ndi siliva;

16Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zii;

ngati makanda osaona kuunika.

17Apo oipa aleka kumavuta;

ndi apo ofooka mphamvu akhala m'kupumula.

18Apo a m'kaidi apumula pamodzi,

osamva mau a wofulumiza wao.

19Ang'ono ndi akulu ali komwe;

ndi kapolo amasuka kwa mbuyake.

20Amninkhiranji kuunika wovutika,

ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima,

21 Chiv. 9.6 wakuyembekezera imfa, koma kuli zii,

ndi kuikumba koposa chuma chobisika,

22wakusekerera ndi chimwemwe

ndi kukondwera pakupeza manda?

23Amuonetseranji kuunika munthu wa njira yobisika,

amene wamtsekera Mulungu?

24Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga;

ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.

25Pakuti chimene ndinachiopa chandigwera,

ndi chimene ndachita nacho mantha chandidzera.

26Wosakhazikika, ndi wosakhala chete, ndi wosapumula ine,

koma mavuto anandidzera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help