1 Aro. 8.24-25 Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
2Aheb. 11.39Pakuti momwemo akulu anachitidwa umboni.
3Gen. 1.1Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zochokera mwa zoonekazo.
4Gen. 4.4-8Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.
5Gen. 5.23-24Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;
6koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
7Gen. 6.13, 22Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.
8Gen. 12.1, 4Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.
9Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;
10Aheb. 13.14pakuti analindirira mudzi wokhala nao maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.
11Gen. 17.19Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;
12Gen. 22.17mwa ichinso kudachokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m'mwamba, ndi ngati mchenga, uli m'mphepete mwa nyanja, osawerengeka.
13 Gen. 23.4; Yoh. 8.56; Aef. 2.19 Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.
14Pakuti iwo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.
15Ndipotu akadakumbukira lijalo adatulukamo akadaona njira yakubwera nayo.
16Eks. 3.6, 15; Mat. 22.32Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ichi Mulungu sachita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.
17 Gen. 22.1, 9 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isaki, ndipo iye mene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha;
18Gen. 21.12amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isaki mbeu yako idzaitanidwa:
19Aro. 4.17, 19, 21poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.
20Gen. 27.27, 39Ndi chikhulupiriro Isaki anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zilinkudza.
21Gen. 48.5, 16, 20Ndi chikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pa mutu wa ndodo yake.
22Gen. 50.24-25Ndi chikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anatchula za matulukidwe a ana a Israele; nalamula za mafupa ake.
23Eks. 2.2-3Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akum'bala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaopa chilamuliro cha mfumu.
24Eks. 2.10-11Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao;
25Mas. 84.10nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;
26Aheb. 13.13nawerenga tonzo la Khristu chuma choposa zolemera za Aejipito; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho.
27Eks. 10.28-29Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.
28Eks. 12.21-28Ndi chikhulupiriro anachita Paska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.
29Eks. 14.22, 29Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.
30Yos. 6.20Ndi chikhulupiriro malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.
31Yos. 6.23Ndi chikhulupiriro Rahabu wadama uja sanaonongeka pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.
32Ower. 4.6; 6.11; 13.24; 11.1; 1Sam. 16.1, 13; 20.1Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri;
33Dan. 6.22mene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa mikango,
34Ower. 15.8; 1Sam. 20.1; Yob. 42.10; Dan. 3.25nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.
351Maf. 17.22; Mac. 22.25Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,
36Gen. 39.20kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende;
37Mac. 7.58anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa,
381Maf. 18.4(amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.
39Aheb. 11.2, 13Ndipo iwo onse adachitidwa umboni mwa chikhulupiriro, sanalandira lonjezanolo,
40Aheb. 8.6popeza Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu opanda ife.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.