LEVITIKO 23 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za nyengo zoikika za Yehova

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.

3Eks. 23.12; Luk. 13.14Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.

Paska

4Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, masonkhano opatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.

5Eks. 12.18; Yos. 5.10; 1Ako. 5.7Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, pali Paska wa Yehova.

6Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa.

7Tsiku lake loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena.

8Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

Zipatso zoyamba

9Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

101Ako. 15.20Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;

11ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata Sabata wansembe aweyule.

12Ndipo tsiku loweyula mtolowo, ukonze mwanawankhosa wopanda chilema, wa chaka chimodzi, akhale nsembe yopsereza ya Yehova.

13Ndipo nsembe yaufa yake ikhale awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, ichite fungo lokoma; ndi nsembe yake yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.

14Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza nacho chopereka cha Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse.

15Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wansembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu;

16Mac. 2.1muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lachisanu ndi chiwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano.

17Mutuluke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi chotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.

18Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, anaankhosa asanu ndi awiri, opanda chilema a chaka chimodzi, ndi ng'ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.

19Mukonzenso mwanawambuzi mmodzi akhale nsembe yauchimo, ndi anaankhosa awiri a chaka chimodzi akhale nsembe yoyamika.

20Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi anaankhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.

21Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.

22 Lev. 19.9 Ndipo pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.

23Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

24Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.

25Musamagwira ntchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova.

Tsiku la chitetezero

26Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

27Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.

28Musamagwira ntchito iliyonse tsiku limenelo; pakuti ndilo tsiku la chitetezero, kuchita chotetezera inu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake.

30Ndi munthu aliyense wakugwira ntchito iliyonse tsiku limenelo, ndidzaononga munthuyo pakati pa anthu a mtundu wake.

31Musamagwira ntchito iliyonse; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.

32Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzichepetse; tsiku lachisanu ndi chinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.

Chikondwerero cha Misasa

33Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

34Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri pali chikondwerero cha Misasa ya Yehova, masiku asanu ndi awiri.

35Tsiku loyamba likhale msonkhano wopatulika, musamagwira ntchito ya masiku ena.

36Yoh. 7.37Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lachisanu ndi chitatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira ntchito ya masiku ena.

37Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lakelake;

38pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zowinda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.

39Koma tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutatuta zipatso za m'dziko, muzisunga chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lachisanu ndi chitatu mupumule.

40Ndipo tsiku loyambali mudzitengere nthambi za mitengo yokoma, nsomo za kanjedza, ndi nthambi za mitengo yovalira, ndi misondodzi ya kumtsinje; ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu masiku asanu ndi awiri.

41Ndipo musunge chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri m'chaka; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; musunge mwezi wachisanu ndi chiwiri.

42Neh. 8.14-16Mukhale m'misasa masiku asanu ndi awiri; onse obadwa m'dziko mwa Israele akhale m'misasa;

43kuti mibadwo yanu ikadziwe kuti ndinakhalitsa ana a Israele m'misasa, pamene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

44Ndipo Mose anafotokozera ana a Israele nyengo zoikika za Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help