MASALIMO 94 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu wolungama adzaweruza oipa

1 Deut. 32.35 Mulungu wakubwezera chilango,

Yehova, Mulungu wakubwezera chilango, muoneke wowala.

2 Mas. 7.6 Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi:

Bwezerani odzikuza choyenera iwo.

3Oipa adzatumpha ndi chimwemwe kufikira liti, Yehova?

Oipa adzatero kufikira liti?

4Anena mau, alankhula zowawa;

adzitamandira onse ochita zopanda pake.

5Aphwanya anthu anu, Yehova,

nazunza cholandira chanu.

6 Yes. 10.1-2 Amapha wamasiye ndi mlendo,

nawapha ana amasiye.

7Ndipo amati, Yehova sachipenya,

ndi Mulungu wa Yakobo sachisamalira.

8 Mas. 92.6 Zindikirani, opulukira inu mwa anthu;

ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?

9 Eks. 4.11 Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva?

Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya?

10 Yes. 28.26 Kodi Iye wakulangiza mitundu ya anthu, ndiye wosadzudzula?

Si ndiye amene aphunzitsa munthu nzeru?

11 1Ako. 3.20 Yehova adziwa zolingalira za munthu,

kuti zili zachabe.

12 Yob. 5.17; Aheb. 12.5-6 Wodala munthu amene mumlanga, Yehova;

ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu;

13kuti mumpumitse masiku oipa;

kufikira atakumbira woipa mbuna.

14 1Sam. 12.22; Aro. 11.1-2 Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake,

ndipo sadzataya cholandira chake.

15Pakuti chiweruzo chidzabwera kunka kuchilungamo,

ndipo oongoka mtima onse adzachitsata.

16Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa?

Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?

17 Mas. 124.1-2 Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova,

moyo wanga ukadakhala kuli chete.

18Pamene ndinati, Litereka phazi langa,

chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.

19Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga,

zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

20 Amo. 6.3 Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza,

wakupanga chovuta chikhale lamulo?

21 Mat. 27.1, 4 Asonkhana pamodzi pa moyo wa wolungama,

namtsutsa wa mwazi wosachimwa.

22 Mas. 62.2, 6 Koma Yehova wakhala msanje wanga;

ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.

23 Miy. 5.22 Ndipo anawabwezera zopanda pake zao,

nadzawaononga m'choipa chao;

Yehova Mulungu wathu adzawaononga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help