EKSODO 30 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za guwa la nsembe lofukizapo

1Ndipo upange guwa la nsembe la kufukizapo; ulipange la mtengo wakasiya.

2Utali wake ukhale mkono, ndi kupingasa kwake mkono; likhale laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zituluke m'mwemo.

3Ndipo ulikute ndi golide woona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolide pozungulira.

4Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.

5Ndipo upange mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide.

6Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.

71Sam. 3.3Ndipo Aroni azifukizapo chofukiza cha zonunkhira zokoma m'mawa ndi m'mawa, pamene akonza nyalizo, achifukize.

8Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, achifukize chofukiza chosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu.

9Lev. 10.1Musafukizapo chofukiza chachilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa; musathirepo nsembe yothira.

10Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.

Ndalama za chiombolo

11Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

12Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.

13Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.

14Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zake, apereke choperekacho kwa Yehova.

15Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.

16Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.

Za mkhate wakusambiramo

17Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti,

18Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa chihema chokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

19Ndipo Aroni ndi ana ake amuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao;

20pakulowa iwo m'chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;

21asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.

Za mafuta odzoza opatulika

22Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti,

23Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,

24ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;

25ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa machitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.

26Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni,

27ndi gomelo ndi zipangizo zake zonse, ndi choikapo nyali ndi zipangizo zake,

28ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lake.

29Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.

30Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake amuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe.

31Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu.

32Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.

33Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.

Za chofukiza

34Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi lubani loona; miyeso yofanana;

35ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosanganiza mwa machitidwe a wosanganiza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika;

36nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.

37Koma za chofukizacho uchikonze, musadzikonzere nokha china, mwa makonzedwe ake amene; muchiyese chopatulika cha Yehova.

38Aliyense wokonza china chotere kununkhizapo, asadzidwe kwa anthu a mtundu wake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help